Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Kalisto Pasuwa wati ali ndichikhulupiliro kuti timu yake iyambaso kuchita bwino mu Super League masana ano pamene akukumana ndi timu FOMO pabwalo la Kamuzu.
Bullets, yomwe ikuteteza ukatswiriwu, yasewera masewero 12 ndipo yapambana masewero atatu, kufanana mphamvu kasanu ndi katatu komanso kugonja kamodzi.
Timuyi ili panambala 6 ndi 17 points pamene FOMO ili panambala 12 ndi 14 points.
Masewerowa aonetsedwa pakanema wa MBC.
Mumasewero ena amene achitike masanawa, Creck Sporting Club ikumana ndi Civil Service United pabwalo la Civo pamene MAFCO isewera ndi Karonga United pabwalo la Chitowe.
Olemba: Praise Majawa