Apolisi ku Bunda m’boma la Lilongwe agwira anthu awiri powaganizira kuti adapha mlamu wawo, a Luciano Masiye a zaka 26, pomumenya ndikukwilira thupi lake ku manda.
Izi akuti zidachitika usiku wapa 10 mwezi uno pamudzi wa Lumwila, mdera la mfumu yaikulu Chadza m’bomali.
Awiriwo akhala akubisala kwa sabata ziwiri.
Malinga ndi ofalitsankhani wa apolisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu, anthuwa ndi a Polofesa Posiyano a zaka 24 komanso a Stephano Kwalapu a zaka 27.
A Chigalu ati malemu Masiye adapita pamudzipo kuti akakambirane ndi mkazi wake yemwe adasiyana naye ndikukwatira mkazi wina mwezi wa February chaka chino.
Koma zokambirana zawo akuti sizidaphule kanthu ndipo adayamba kuononga wina mwa katundu pakhomopo.
Pa chifukwachi, mkazi wawo adakuwa ndipo azichimwene akewa adafika ndikuyamba kumumenya mkuluyo mpaka kumupha.
A Chigalu ati usiku omwewo awiriwo anaika kumanda thupi la malemuyo osadziwitsa akuluakulu m’mudzi komanso achibale.
Komabe nkhaniyi inadziwika ndipo amfumu anakadziwitsa apolisi, amene anagwira m’modzi mwa oganiziridwa, a Azele Kaiteni azaka 38, amene adalondolera apolisi pomwe adakwilira malemuyo.
Anthu atatu onsewa akuyembekezeka kukayankha mlandu wakupha ku khothi posachedwapa.