Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe yapempha mzika zake kukhala adindo pa ntchito yosamala misika yosiyanasiyana ya mumzindawu.
Mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a Esther Sagawa, ndi imene yapereka pempholi pamene khonsoloyi imalandira zipangizo kuchokera ku kampani ya Waste Advisers, imene yapereka ndi kuyika malo otayola zinyalala (waste bins) okwana 100.
A Sagawa anati ndikofunika kuti anthu ayambe kuzindikira udindo wawo komanso kutenga nawo gawo losamalira misikayi popewa kutaya zinyalala mwachisawawa kuti idzikhala yaukhondo.
Mkulu oyendetsa ntchito za Waste Advisers, a John Chome, anati ndi khumbo lawo kuona misika ndi mizinda ya dziko lino ili yosamalika komanso yochititsa kaso.
Ntchitoyi ayikhazikitsanso m’zigawo zonse za dziko lino ndipo ndiya ndalama zokwana K12 million, pansi pa mutu wakuti ‘Khalani aukhondo, tayani zinyalala zanu moyenera’.