Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Pali kusintha kwina pa programme — Kunkuyu

Nduna yazofalitsa nkhani yalengeza kusintha kwina kwa ndondomeko ya momwe mwambo wa maliro a Dr Saulos Chilima uyendere.

Mwa zina, a Kunkuyu ati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera atsogolera mwambo wotenga thupi la Dr Chilima ku nyumba ya chisoni nthawi ya 1 koloko masana ndipo akakhala nawo pa ulendo opita ku tchalitchi ya St. Patrick’s ku Area 18 ku Lilongwe, komwe kukakhale mwambo wa mapemphero.

Malinga ndi a Kunyuyu, kuchoka ku tchalitchi thupi la Dr Chilima likakhala kunyumba kwawo ku Area 12, malinga ndi pempho la akubanja ndipo akakhala kumeneko mpaka loweruka mmawa.

Loweruka, Dr Chakwera akatsogolera mwambo wotenga  thupi la Dr Chilima kupita nalo ku nyumba ya Malamulo komwe kukakhale   mwambo wa mapemphero ndipo anthu osiyanasiyana akakhala ndi  mwayi opereka ulemu otsiriza kwa Dr Chilima.

Thupi la Dr Chilima likakhala kunyumba yamalamuloyi mpaka lamulungu mmawa, komwe mtsogoleri wa dziko lino akatsogolerenso mwambo otenga malemuwa kupita ku Bingu National Stadium, kumene anthu akakhale ndi mwayi opereka ulemu kwa wachiwiri Kwa mtsogoleri wa dziko linoyu.

Kuchoka uko, thupi la Dr Chilima akalitengera kumudzi kwawo ku Nsipe komwe akaliyike mmanda lolemba.

Pa msonkhano wa atolankhaniwu, a Kunkuyu ati agwiritsa ntchito zina zomwe zikulembedwa mmasamba a mchezo mukafukufuku yemwe akuchitika  koma apempha onse omwe ali ndi uthenga osiyanasiyana kuti apite nawo kwa  anthu oyenera  mmalo mopita nawo mmasamba a mchezo.

Iwo apemphanso  anthu osiyanasiyana omwe akuyankhula zosiyanasiyana kuti asatengelepo mwayi opanga ndale pa maliro a Dr Chilima.

Iwo atsindika kuti  kubanja ati  sakufuna kuti pa malirowa pakhale za ndale.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

ESCOM set to offer internet services

Rabson Kondowe

Kachere Rehabilitation Centre calls out for help

MBC Online

New Anti-Money Laundering Policy launched

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.