Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local News Nkhani

Ophunzira a ulumali asamadziyang’anire pansi — Mkuonera

Unduna wa zamaphunziro walangiza ophunzira omwe ali ndi ulumali kuti asamadziyang’anire pansi chifukwa nawo ali ndi kuthekera kochita bwino.

M’neneri ku undunawu, a Mphatso Mkuonera, amayankhula izi m’boma la Kasungu pamene amayendera ntchito yomanga zipinda zophunzilira, za sayansi komanso zowerengerako mabukhu zomwe zili pansi pa ntchito ya Equity with Quality Learning at Secondary (EQUALS).

Atafika pa Sekondale ya Kasungu, a Mkuonera anakumana ndi achinyamata amene ali ndi khungu la chi alubino ndipo iwo anati boma likumanga zithu zambiri zokhudza maphunziro zomwe ndi zokomera onse m’dziko muno pakusatengera ulumali.

Ntchito ya EQUALS ikulandira thandizo kuchokera ku World Bank.

 

Related posts

MFC champions sustainable fertilizer usage in Malawi

Rabson Kondowe

MoH calls for improved dental services

Rabson Kondowe

Dr Chakwera adzudzula anthu opondereza pa ntchito ya mtukula pakhomo

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.