Anthu ochita malonda m’misika ya mchigawo chakum’mawa apempha mtsogoleri wadziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, kuti boma liwathandize kudzera mu ngongole zoti zithandize kukwezanso mabizinesi awo, amene adagwa chifukwa chamavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo n’gamba.
Ochita malondawa ayankhula izi ku Nyumba ya Boma ya Chikoko Bay m’boma la Mangochi pankumano umene Prezidenti Chakwera anayitanitsa ochita malonda osachepera 300 kuti amve mavuto amene akukumana nawo.
Malinga ndi wapambando wa ochita malonda ochokera ku Liwonde, a Daniel Bandawe, ambiri akulakalaka atepeza ngongole kuti ntchito zawo zamalonda zipite patsogolo.
Mwazina, ochita malondawa adandaulanso ndi kuwonongeka kwa misika komanso misewu zomwe zikupangitsa kuti ntchito za malonda zivute m’madera ambiri.
Mtsogoleri wa dziko lino poyankhapo wati wamva madandaulowo ndipo achita chotheka kuti afikire akuluakulu okhudzidwa kuti ochita malondawa athandizike.
Olemba: Mirriam Kaliza