Khoti la Magistrate ku Phalombe lalamula nyakwawa Nayuma, yomwe dzina lake ndi Leonard Julius, kukakhala kundende zaka 12 chifukwa chogwililira mtsikana wazaka 14.
Mneneri wapolisi ku Phalombe, Jimmy Kapanja, wati izi zinadziwika mwezi wa October chaka chatha.
Malinga ndi a Kapanja, pakadali pano mtsikanayo, yemwe amadwala matenda a mu ubongo, ali ndi mwana wa nyakwawayo.