Khoti lina ku Balaka lalamula bambo wazaka 45, Frank Nazombe, kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana K65,000 chifukwa chonyoza mayi wodwala matenda a AIDS.
Mneneri wapolisi ku Balaka, a Gladson M’bumpha, wati Nazombe anayambana ndi mayiyo ku mowa.
Tsiku lotsatira, Nazombe analawira mammawa kupita kunyumba kwa mayiyo ndikuyamba kumunena kuti akudwala matenda a AIDS ndipo wafalitsa matendawo kwa amuna ochuluka mderalo.