Malawi Broadcasting Corporation
Health Local Nkhani

Ntchito yoyika makina opanga mpweya pa chipatala cha Mzuzu Central yachedwa

Komiti ya mtsogoleri wa dziko lino yoona za matenda a COVID-19 ndi cholera yapempha amene akugwira ntchito yoyika makina opanga mpweya pa chipatala chachikulu cha Mzuzu Central kuti agwire ntchitoyi mwamsanga komanso mwadongosolo.

Wapampando wa komitiyi, Dr Wilfred Chalamila Nkhoma, ndi omwe apereka pemphori kwa omwe akugwira ntchito yoyika makina komanso zomangamanga pa malowa, yomwe akuigwira ndi ndalama zochokera ku Global Fund.

Ntchitoyi imayenera kutha mmwezi wa October chaka chatha koma izi sizili chomwechi kaamba ka mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo kuitanitsa zipangizo kunja kwa dziko lino.

Polankhula ndi omwe akugwira pa malowa, a Chalamila Nkhoma ati ndi zokhumidwitsa kuti ntchitoyi sinathe kufika lero.

Mmau ake, mkulu wa chipatala cha Mzuzu Central, Dr John Chipolombwe, wati ali ndi chikhulupiliro kuti malowa ayamba kugwira ntchito yake mwezi wa mawa ndipo izi zithandiza chipatalachi kupulumutsa ndalama za nkhaninkhani zomwe akugwiritsa ntchito kugula mpweyawu malo ena ndi ena.

 

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tambala Super Cup ayikhazikitsa

MBC Online

Malawi earmarked for phase 3 of TB vaccine trial

MBC Online

Community spirit shines in schoolblock project

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.