Kampani ya Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) yati $21 million yomwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chalwera anakatenga ku msonkhano wa COP27 ithandizira kugulira zida zamakono zosungira mphamvu ya magetsi a dzuwa.
Izi zikudza pamene kampani za ESCOM ndi Electricity Generation Company (EGENCO) zikufunitsitsa kuonjezera mphamvu zamagetsi m’dziko muno popeza kampanizi zataya magetsi ambiri kaamba ka umbava wazida zofunikira.
Mkulu wa EGENCO, a Maxon Chitawo, wati chidwi chawo chili pofuna kupanga mphamvu zamagetsi zosachepera 2000 megawatts pofika chaka cha 2040.
A Chitawo ati, pakadali pano, bungweli likukumana ndi mikwingwirima monga ngozi zakudza kaamba kakusintha kwa nyengo komanso kuwonongeka kwa makina opangira mphamvu zamagetsi ku Kapichira, Nkula komanso Tedzani.
Iwo ati dongosolo lokhazikitsa malo atsopano opangira mphamvu zamagetsi m’ma boma a Salima ndi Nkhotakota liri m’chimake.
Pakadalipano, dziko la Malawi linamaliza ntchito yonse yofuna kutenga mphamvu zamagetsi zokwana 50 megawatts kuchokera m’dziko la Mozambique kumene kwatsala kuti amalizitse.

