Bungwe la Save the Children lati ntchito za maphunziro ndi umoyo wabwino m’sukulu za m’dziko muno zikufunika kuunikidwa ndikukonzedwanso mwakuya komanso mwamakono pofuna kuthana ndi mabvuto akusachitabwino kwa ophunzira ambiri pa maphunziro.
Bungweli lanena izi pomwe limapereka zotsatira za kafukufuku wake pa momwe ndondomeko ya boma ya maphunziro ndi umoyo yakhala ikuyendera chiikhazikitsire m’chaka cha 2009.
Mkulu owona za ntchito ndi maubale ku bungweli, Chakufwa Munthali ati ngakhale ntchitoyi yayenda bwino, yakumana ndizotsamwitsa zambiri monga kusowa kwa chakudya, zipangizo zaukhondo monga zimbuzi komanso madzi aukhondo m’sukulu zambiri, maka za m’madera akumidzi.
A Munthali ati Save the Children kudzera mu ndondomeko yake ya za maphunziro ndi umoyo ipitilira kuunikira ndikuthandiza boma pa ntchitoyi ndipo apempha umodzi pakati pa aphunzitsi komanso makolo poyang’anira bwino anawa.
Wachiwiri kwa mkulu oyendetsa ndondomeko za maphunziro ndi umoyo ku unduna wa maphunziro, a Maguza Tembo, anagwirizana ndi zotsatira zakafukufukuzi zomwe ati zithandiza kwambiri pa ntchito yokonzanso ndondomekoyi.