Nthambi yoona zanyengo m’dziko muno yachenjeza kuti namondwe akhoza kubuka lamulungu lino panyanja yamchere pakati pa mayiko a Madagascar ndi Mozambique ndipo ali ndikuthekera kofalikira m’chigawo chakummwera kwa dziko lino.
Kudzera mukalata imene nthambiyi yatulutsa, iyo yatinso madera ambiri apitilira kulandira mvula yochuluka ndipo yalangiza anthu kuti apewe kuwoloka mitsinje yodzadza ndikukhala tcheru chifukwa madzi akhoza kusefukira madera ochuluka.
Izi zikudza pamene madzi osefukira asautsa anthu mmaboma a Nkhotakota ndi Karonga.
Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akuyembekezeka kuyendera ena mwa anthuwa ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota.