Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

NRFA Simso-Mzuzu 12 yatentha

Songwe Border United yaonjezera mwayi okhala akatswiri a mpikisano wa NRFA Simso-Mzuzu 12 itagongetsa timu ya Jenda United 2-0 dzulo pa bwalo lamasewero la Kangindwa m’boma la Karonga.

Thompson Manyowa ndi amene anamwetsa zigoli zonse muchigawo chachiwiri.

Pamndandanda wamatimu a ligiyi, Songwe Border United tsopano ikutsogola ndi mapoint 24 pamasewero khumi, Chintheche ndi yachiwiri ndi mapointi 19 pamasewero ngati omwewo, ndipo Raiply ndi imene ikutsatira pachitatu ndi ma point 18. Jenda ndiyachinayi ndi mapointi 16 atasewera masewero 11.

Mphunzitsi wa timu ya Songwe, a Gift Chilongo, wati kupambanaku kuwalimbitsa kuti akhale akatswiri aligiyi chaka chino.

Pamene mlembi wa Jenda United, a Edward Mwale, anati alimbikira mpakana kumapeto ampikisanowu kuti athere pa nambala yabwino.

Wapampando wakomiti yoyendetsa masewero a mpira wamiyendo m’boma la Karonga, a Stain Kakangula, anati mpikisano wa chaka chino ndi olimba kwambiri ndipo pakufunika matimu a ligiyi avale zilimbe.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kalinda health post launched in Dowa

MBC Online

CHOLERA OUTBREAK IN MULANJE

Mayeso Chikhadzula

CHILIMA CHARGED WITH 6 COUNTS OF CORRUPTION

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.