Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

NRB yalemba anthu opyola 12 million

Bungwe la National Registration Bureau (NRB) yalemba anthu oposa 12 million mukaundula wa nzika za dziko lino.

Ichi ndi chiwerengero chokwera poyerekeza ndi anthu 11.6 million omwe bungwe la National Statistical Office lidasindikiza m’chaka cha 2018 amene ali opitilira zaka 16 zakubadwa.

Bungweli lati lalembanso mu kaundula ana obadwa kumene oposa 3.2 million, zomwe zikutanthauza kuti ndi 76% ya anthu m’dziko muno amene alembedwa mu kaundulayu.

Mlembi wa mkulu ku NRB, a Mphatso Sambo, ati bungwe lawo liyambanso kalembera wina, yemwe m’chingerezi akumutchula kuti “mop-up” m’madera onse a m’dziko muno.

A Sambo apemphanso achinyamata omwe adalembedwa kuti aphunzire ntchito (internship) kuti asachite zionetsero zili zonse kaamba kakuti zichedwetsa ntchito yotumikira anthu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Azimayi sakugwiritsa ntchito makondomu achizimayi

Simeon Boyce

Bushiri wagawa chimanga kwa anthu oposa 18,000

Eunice Ndhlovu

Wina wapambananso!

Jeffrey Chinawa
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.