Makhansala awiri a chipani cha Democratic Progressive (DPP) atuluka mchipanichi ndipo alowa cha Malawi Congress (MCP).
Mkulu okopa anthu mu MCP a Moses Kunkuyu alandila makhansala awiriwa pa msonkhano omwe anachititsa pa sukulu ya Chilayeni m’dera la Sub TA Nyambalo ku Phalombe.
Makhansalawa ndi a Felix Blair Jumbe a Mauzi ward mdera la Phalombe North East, komanso a Fedison Thomas a dera la Likulezi Ward kum’mwera kwa Phalombe.
Makhansalawa omwe anabwela ndi mafumu a m’maderawa ati achita izi kaamba Prezidenti Dr Lazarus Chakwera ndi okhululuka komanso chipani chawo ndi cha mtendere ndipo akufuna chitukuko.