Bungwe la Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA) latsutsa kafukufuku wa sukulu ya ukachenjede ya m’dziko la Ethiopia lomwe linati dziko la Malawi muli chiwerengero chachikulu cha mankhwala osavomerezeka komanso olowa mwa chinyengo mu Africa.
Mkulu wa bungweli, a Mphatso Kawaye, ati kafukufukuyi ndi wam’chaka cha 2015 ndipo sakuyimira mankhwala onse kaamba kakuti analunjika pa mankhwala a Malungo a mu zipatala zomwe sizaboma.
“Zitha kutheka kuti kasamalidwenso kamankhwalawa kanali kovuta kaamba koti zotsatira zamankhwala omwe anayeza zimasiyanasiyana ndipo ndizovuta kuzikhulupilira ,” anatero a Kawaye.
M’modzi mwa akulu ku unduna wazaumoyo, a Godfrey Kadewere, ati boma pamodzi ndi PMRA akuyesetsa powonetsetsa kuti mankhwala m’zipatala ndi ovomerezeka komanso sakupereka chiopsezo pa umoyo wa anthu.