Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports

Nkhonya ya Hannock Phiri ndi Regene Champion ikununkhira

Nkhonya ya mtima bii yomwe ikuyembekezeka kuchitika pa 5 October pakati pa katswiri wakuno ku Malawi Hannock Phiri ndi chiphona chaku DRC Regene Champion tsopano yayamba kununkhira.

Kampani yomwe yakonza nkhonyayi ya New Dawn Boxing Promotion ikupitilira kupeza thandizo kuchokera kwa abwenzi omwe ikuchitanawo ubale.

Lero, kampani ya PLMB yapereka K3.5 million ku New Dawn zothandizira zokonzekera masewerowa, omwe adzachitikire mkati mwa Bingu International Convention Centre ku Lilongwe.

Mkulu ofalitsankhani ku kampani ya PLMB Engineering Happy Boko wati akufuna kuthandiza amene ali ndi chidwi chotukula masewero osiyanasiyana m’dziko muno, kuphatikizapo a nkhonya.

Mmodzi mwa akuluakulu a New Dawn Boxing, Brighton Mwando, wathokoza kampaniyi kamba kathandizoli, lomwe wati labwera munthawi yake kuti anyamatawa akinzekere bwino ndikudzapereka masewero apamwamba kwa a Malawi.

By Amin Mussa & Foster Maulidi

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tipereke mpata kwa ena opata mphoto – Mandota

Emmanuel Chikonso

Financial institutions urge construction players to explore funding opportunities

MBC Online

CHAKWERA FOR BETTER WELFARE OF TRADITIONAL LEADERS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.