Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani Sports Sports

Nkhondo ya mphunzitsi ndi ophunzira wake

Masana ano matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers akhala akuthambitsana pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Chochititsa chidwi ndi chakuti mphunzitsi wa timu ya Bullets, Calisto Pasuwa, akhala akuonana maso ndi maso ndi omuthandizira wake wakale yemwe tsopano ndi mphunzitsi wa timu ya Silver, Peter Mponda.

Poyankhulapo, timu ya FCB Nyasa Big Bullets yati ilibe zifukwa zokhala ndi phuma pamene iwo akuyembekezera kuti timu ya Silver Strikers idzola zigoli pamasewerowa.

Mphunzitsi wa timuyi, a Calisto Pasuwa, anati pamasewerowa iwo ayesetsa kuchilimika kuti osewera awo akhale ndi maganizo a bwino.

A Pasuwa anati izi zilichomwechi chifukwa matimu amu ligi yayikulu amalimbikira koposa akamakumana ndi Bullets zomwe zimapangitsa kuti masewero alionse akhale ovuta.

Iwo anatinso osewera awo ena odalilika ndi ovulala komanso akuyenereka kukonza kutsogolo kwawo kuti azimwetsa zigoli mosavuta.

Poyankhulapo, Mphunzitsi wa timu ya Silver Strikers, a Peter Mponda, ati ndi okonzeka ngakhale akudandaula pang’ono chifukwa osewera awo ena anapita kukatumikira timu ya pfuko (Flames) komanso ali ndi osewera angapo omwe ndi ovulala.

A Mponda ati iwo ayesetsa kuti atolele ma point atatu pamasewerowa komabe sikuti kupambana kulozera tsogolo la ligiyi.

Koma, mphunzitsiyu anatinso masewero amenewa sakhala ophweka chifukwa Bullets imakhala ya mphamvu kwambiri ikamasewera pa bwalo la Kamuzu, ndipo malingana ndi mbiri, timuyi sidagonjeko pa bwalopa kuyambila m’chaka cha 2021.

Silver Strikers, yomwenso imadziwika kuti ‘Mabanker’ ili pa mwamba pa m’ndandanda wa matimu amu ligi yayikulu ndi ma point 22 pamasewero 8. Pomwe timu ya FCB Nyasa Big Bullets, yomwe amaitchanso kuti ‘Maule’ ndi yachisanu ndi ma point 14.

Aka kakhala kachitatu kuti timu ya Mabanker isewere koyenda atasewera ndi Dedza Premier Bet Dynamos komanso Baka City.

M’masewero awo a m’mbuyomu, Mabanker anagonjetsa matimu a Creck Sporting 2-0, Mighty Mukuru Wanderers 2-0 ndi Karonga United 4-2.

Mbali inayi, Maule akhala akusewera masewero awo achisanu pakhomo.

Bullets ikuchokera kofanana mphamvu ndi Moyale Barracks 0-0, inagonjetsa Mzuzu City Hammers 2-0 ndipo inafanana mphamvu ndi ma timu a MAFCO ndi Wanderers 1-1, masewero onsewo.

Mu mwezi wa March, matimuwa anakumanaponso mu mpikisano wa chikho cha Charity Shield ndipo mu mphindi 90 zonse sanamwetsane zigoli ndipo masewerowa anathera kuwaya pamene Bullets inapweteka Silver 7-6 ndi kutenga chikhochi.

Chaka chatha mu ligiyi, awiriwa anafanana mphamvu 1-1. Bullets ndi imene ikusungira chikho cha ligiyi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MACRA’S CERT VOWS TO TACKLE CYBER THREATS

Alinafe Mlamba

Phwando la mayimbidwe auzimu likhalaponso ku Blantyre

Paul Mlowoka

GSMA HAILS MALAWI’S DIGITALISATION EFFORTS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.