Polisi ya Lingadzi mu mzinda wa Lilongwe yamanga msungwana wazaka 17 zakubadwa, yemwe sadatchulidwe dzina, pomuganizira kuti anapha mwana wazaka 10 pofuna ku kondweretsa bwenzi lake lapatsamba la mchezo yemwe dzina lakenso silikudziwika.
Ofalitsa nkhani pa polisiyi, a Cassim Manda, ati bwenzi la msungwanayo limamkakamiza kuti azimujambulila kanema olaula komanso kuti azichita zadama ndi amuna.
A Manda ati bwenzilo linaopseza mtsikanayo kuti abale ake onse amwalira mosamvetsetseka ngati sapereka msembe ya mwana zomwe zinamuchititsa kuti aphe mwana wa okhala moyandikana nawo pa malo ena ogona alendo ku Mtandile mu mzinda omwewo.
Mtsikanayo akumuganizira kuti atapha mwanayu anabisa thupi lake pansi pa bed pa malo ogona alendowa ndipo ogwira ntchito ku malowa ataona izi anawuza a polisi amene anafufuza mtsikanayu kudzera pa lamya yake ya m’manja yomwe anayimbira malowa kuti agule chipinda.
Mtsikanayu amachokera m’mudzi mwa Chamba 2, kwa mfumu yayikulu Malengachanzi m’boma la Nkhotakota ndipo akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.