Malawi Broadcasting Corporation
Development Education Local Local News Nkhani

Malawi ndi mgodi wazambiri — SMASE

Bungwe la Strengthening Science and Mathematics Education in Africa (SMASE) lati dziko la Malawi lili ndi kuthekera kokhala mphika waza ulimi mu Africa pokhapokha patakhala ndondomeko yamaphunziro oyenerera.

Ena mwa auluakulu a bungweli, amene ndi ochokera ku unduna wa zamaphunziro m’dziko la Zambia, anayankhula izi pamene anali ndi zokambirana ndi nduna ya zamaphunziro a pamwamwamba, a Jessie Kabwila, munzinda wa Lilongwe.

Dr Benson Banda, amene akutsogolera komiti ya SMASE, anati zimene awona m’dziko lino ku Zambia kulibe.

“Ndinali odabwa kuti ku Malawi utha kudzuka ndi kumeta nthawi ina iliyonse. Kwathu kulibe magetsi otere,” a Banda anatero.

Iwo anati Malawi ili ndi madzi ochitira ulimi wa mthilira ndipo enanso atha kumagulitsanso m’mayiko ena monga umo lichitira dziko la Lesotho.

A Kabwila anayamikira kubwera kwa bungweli ndipo anati izi zikusonyeza ubale wa bwino umene ulipo ndi mayiko ena chifukwa ndi zofunikira kuchitukuko cha dziko lino.

Dziko la Malawi likuyembekezeka kuchititsa msonkhano okhudza phunziro la masamu ndi sayansi wamayiko 31 a mu Africa m’ mwezi wa November.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Insufficient resources hinder child labour rehab initiative

MBC Online

All set for Wazisomo Thank You Concert

MBC Online

Limbikani ntchito titukule dziko lathu – Dr Usi

Secret Segula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.