Synod ya Blantyre ya Mpingo wa CCAP tsopano yaonjezera chiwerengero cha abambo omwe ndi mamembala a Utumiki wa Abambo, potsatira kupatulidwa kwa gulu la abambo omwe awalandira ku mpingo wa Manase CCAP mu mzinda wa Blantyre.
Nduna ya zofalitsa nkhani omwenso ndi mneneri wa boma a Moses Kunkuyu ndi mmodzi mwa mamembala atsopano a Utumiki wa a Bambo mu Synod ya Blantyre.
Polankhula pa mwambo opatula mamembala atsopanowo, m’busa Evance James Kapulula omwe amatumikira pa Manase CCAP anati kukhala ndi membala wa Utumiki wa Abambo yemwenso ndi nduna ya boma ndi chisonyezo chachikulu pa kudalirana komwe kulipo pakati pa mpingo ndi boma pa ntchito yosamalira a Malawi.
A Kunkuyu omwe anakhalako Mlembi wa mpingo wa Manase CCAP kawiri ati kupatulidwa kwawo n’kukhala mu Utumiki wa Abambo kwapereka
chilimbikitso pa ntchito yotumikira pa Chikhristu mu Synod ya Blantyre.