Hope Msukwa, amene ndi wa zaka 18, wapambana pa mpikisano okwera njinga zamoto kumapiri aku Misuku m’boma la Chitipa.
Iyeyu wapambana atayendetsa njinga yamoto kwa mphindi 47 pa mtunda wama kilometre 48 ndipo wapeza mphoto ya K1.4 million komanso wagonjetsa anyamata ena oposa 49 amene amapikisana nawo.
Hope anati agwiritsa ntchito ndalamayo kuti agule njinga yake chifukwa imene amagwiritsa ntchito pa mpikisanowo ndi yobwereka.
Thokozani Kanyika ndi amene wakhala wachiwiri ndipo walandira K900,000 pamene Zakaria Kaini wathera pachitatu ndipo walandira K615,000.
Olemba: Hassan Phiri