Mneneri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), Shepherd Bushiri, wadzudzula mchitidwe olanga ana mopitilira muyeso akalakwitsa, ponena kuti izi ndi nkhanza.
Iwo anena izi pamene amagulira katundu osiyanasiyana mwana wa mmudzi mwa Mndola, Mfumu yaikulu Kambwiri m’boma la Salima, amene anadyetsedwa dowe wamuwisi ochuluka masiku apitawa atagwidwa akuba m’munda.
Mneneriyu wati nkhani ya mwanayu ndiyomvetsa chisoni ndipo walonjeza kuti amuthandiza kuti achite maphunziro ake ndikudzakhala mzika yodalirika.
Katundu yemwe amugulirayu ndikuphatikizapo zovala,nsapato komanso zofunda.
Anthu osiyanasiyana, kuphatizikapo bungwe la Malawi Human Rights Commission, adzudzula amene anachitira nkhanza mwanayu ndipo apempha boma kuti lilowelerepo.