Mlimi wa ku Blantyre, a Mariko Kalima, wayiphula pamene wapata K2.5 million mu mpikisano wa Tisanje umene ikupangitsa ndi kampani yopanga sopo ya Hirwa General Dealers.
Polankhula pamene kampaniyi imapereka mphothoyi ku Ndirande munzinda wa Blantyre, kudzera kwa kazembe wawo, Emmie Deebo, a Kalima anathokoza kampaniyi ponena kuti ndalama iwathandiza pogula fetereza ndi zipangizo zina za kumunda.
Mkulu owona za malonda ku kampaniyi, a Best Balala, anati anakhazikitsa mpikisanowu pofuna kuthandiza makasitomala awo mu nthawi ino pamene chuma chikuvuta.