Malawi Broadcasting Corporation
Development Floods Local News Nkhani

Mia athandiza mabanja 3000 ndi chakudya ku Chikwawa

Phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Chikwawa Nkombezi, Abida Mia, apereka thandizo la chakudya kwa mabanja okwana 3000 a m’dera lawo amene akhudzidwa ndi njala kaamba ka mphepo ya El Niño yomwe inadutsa m’dziko muno chaka chatha.

Chakudyachi, chomwe chapita ku madera a Sayindi ndi Mphungu m’bomalo, ndi matumba a ufa ndi ndiwo za soya zomwe azipereka mogwirizana ndi bungwe la Moslem World League, thandizo lomwe liri pansi pa ndondomeko ya Drought Disaster Rapid Response Programme.

A Mia ati anachiwona choyenerera kupereka thandizoli chifukwa anthu ambiri kuderali akusowa pogwira chifukwa cha njala yomwe inadza ndi El Niño komanso kusefukira kwa madzi mu mtsinje wa Shire.

Iwo anathokozanso mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pokhazikitsa ndondomeko zosiyanasiyana kuphatikizapo ya Mtukula Pakhomo komanso kumema mabungwe ndi maiko akunja kuti athandize dziko lino pa vuto la njala.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MACODA and EWF orient persons with disabilities on new Disability Act

MBC Online

Ministry of Gender lauds Ecobank for promoting e-payments

Tasungana Kazembe

UNIMA, Huawei sign MoU on human development

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.