Kampani ya Serato Media Group, imene yakhala ikuthandiza kugulitsa nyimbo za Zeze Kingston, yathetsa m’gwirizano ndi oyimbayu patatha zaka zinayi akugwira ntchito limodzi.
Kalata yochokera ku kampaniyo, yomwe ndi ya m’dziko la South Africa, yati mgwirizanowu watha atakambirana ndi Zeze ndipo onse ndi okhutira ndi momwe oyimbayu nyimbo zake zafalikira kummwera kwa Africa komanso kupambana mphoto zambiri.
Izi zukubwera patangodutsa tsiku limodzi Zeze Kingston atakhazikitsa kampani yake yotchedwa Money Making Music.
Olemba: Alufisha Fischer