Bwanamkubwa wa boma la Neno, Rosemary Nawasha, wati adindo m’bomalo akugwilira ntchito limodzi pofuna kuthana ndi mchitidwe owononga zachilengedwe komanso kubwezeretsa chilengedwe .
A Nawasha ayankhula izi pa sukulu ya pulaimale ya Chikonde pomwe khonsolo ya bomali imalipira anthu omwe akugwira ntchito za m’bwezera chilengedwe yomwe imadziwika kuti Climate Smart Enhanced Public Works Programme (CSEPWP) mchingerezi.
Iwo alangiza anthu omwe akugwira ntchitoyi kuti adzigwiritsa ntchito ndalama zomwe akulandirazo mwa dongosolo kuti miyoyo yawo itukuke.
M’boma la Neno, anthu oposa 14,000 ndiwo akugwira ntchitoyi mmadera khumi ndi anayi.
Anthuwa adzilandira K38,400 pakutha masiku 24.
Mwa zina mu ntchitoyi anthuwa akumadzala mitengo komanso kuchita akalozera mmunda pofuna kuteteza kukokoloka kwa nthaka.
Olemba: Naomi Kamuyango