DoDMA, yomwe ndi nthambi yoona za ngozi zakugwa mwadzidzidzi, yatsindikiza za kufunika kwa ndondomeko zopewera ngozi zobwera kaamba ka kusintha kwa nyengo.
Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu a nthambiyi, a Moses Chimphepo, izi zithandizira kuchepetsa mavuto omwe anthu amakumana nawo nthawi ya ngozi.
A Chimphepo amayankhula izi mumzinda wa Lilongwe pamene amakhazikitsa ntchito yothandiza kupewa ngozi zobwera kaamba kakusintha kwa nyengo.
Ntchitoyi ndi ya zaka ziwiri ndipo igwiridwa mogwirizana ndi mabungwe ena akufuna kwabwino monga Malawi Red Cross Society, World Food Programme, Food Agriculture Organisation, European Union ndi Danish Red Cross.
A Paul Turnbull, amene ndi oyimira bungwe la WFP limene limayang’anira za chakudya padziko lonse, ati kupewa ngozi zisadafike kukhoza kuthandiza anthu kukhala ndi chakudya chokwanira chaka chonse.
Mkulu wa Danish Red Cross, a Eva Nicolson, nawo anatsindikiza kuti njira yopeweratu ngozi zoterozi ndi yofunika chifukwa imathandiza kupeputsa ntchito yosamalira anthu omwe akumana ndi mavuto kamba ka ngozizi.