Bungwe la National Aids Commission (NAC) lati abambo 41 pa 100 alionse m’dziko muno samadziwa kuti ali ndi kachirombo Ka HIV komwe kamayambitsa matenda a AIDS.
A Francis Mabedi, omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la NAC, ati izi zili chomwechi kaamba ka kuti abambo ambiri amaopa kupita ku chipatala, zomwe ati ndi zosayenera.
“Abambo ambiri sakhala ndi chidwi chopita ku chipatala kuyerekeza ndi amayi. Nthawi zambiri amachita mantha,” a Mabedi anauza atolankhani mumzinda wa Blantyre.
Malinga ndi kafukufuku wa za umoyo, anthu 1 million ndi amene ali ndi HIV m’dziko muno.
Olemba: Mercy Zamawa
#MBCDigital
#Manthu