Apolisi munzinda wa Zomba amanga a Jessie Mpanira, 35, powaganizira kuti amafuna kulowetsa chamba ku ndende ya Zomba Maximum.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi ya Zomba, a Andrew Mwale, ati mayiyu anapita ku ndendeko kuti akawone mulamu wake amene akugwira ukayidi kwa moyo wake wonse.
Malinga ndi a Mwale, mayiyo anatenga nsima imene anabisamo fodya wamkuluyo.
Monga mwa malamulo, oyang’anira pa ndendepo anayamba kuyiwunika nsimayo asanakayipereke ndipo anazindikira kuti mayi Mpanira anabisa chamba mkati mwa nsimayo.
Amene akuwaganizirawa ndi a m’mudzi wa Duncan, mfumu yayikulu Malemia m’boma la Zomba.