Ligi ya masewero a Darts m’chigawo chapakati yalandira K6 million imene yachokera ku kampani yogulitsa zipangizo zaulimi ndi mankhwala ya SKM trading imenenso asayinirana nayo mgwirizano Loweruka mumzinda wa Lilongwe.
Mkulu wa za malonda ku SKM, a Asante Kagwada, anati adachita chidwi timu ya dziko lino imene inatenga mendulo ya Silver kwa kumpikisano wa maiko amu Africa m’dziko la Eswatini.
Kagwada anaonjezeranso kuti masewerowa ali ndi tsogolo lowala.
Wapampando oyendetsa ligiyi, a Hetherwick Mkudzenje, anati thandizoli liwonjezera mpikisano umene unalipo kale.
Mlembi wamkulu wa bungwe la Darts Association of Malawi, a Chikondi Maleta, anaonetsa kukondwa ndi izi ndipo anapemphanso kampani zina kuti zibwere ndi kutenganawo gawo lotukula masewerowa.