Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Malamulo a chipani akuvomereza atosgoleri ake kudzachita mgwirizano ndizipani zina’

Msonkhano waukulu wa chipani cha People’s (PP) wapereka mphamvu kwa atsogoleri omwe asankhidwe kudzachita mgwirizano ndi zipani zina zomwe adzafune kuyenda nazo limodzi pa chisankho chosankha mtsogoleri wa dziko lino mu September chaka cha mawa.

Nthumwi ku msonkhanowu, womwe wayamba lachisanu mu nzinda wa Lilongwe, zasintha ena mwa malamulo akulu achipanichi, omwe tsopano akupereka mphamvu kwa atsogoleri kudzachita mgwirizano ndi zipani zina.

Nthumwi zayamba kuvota, kusankha anthu m’maudindo osiyanasiyana mu chipanichi. Mtsogoleri wa chipanichi, Dr Joyce Banda, wati adzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko.

Anthu anai omwe akufuna udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi alibe opikisananawo.

Iwo ndi a Ephraim Chibvunde, wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi ku chigawo chakum’mwera, Peter Kamange, wachiwiri kwa mtsogoleri ku chigawo chapakati, Lawrence Bisika, wachiwiri kwa mtsogoleri kumvuma  ndi Duncan Kaonga, wachiwiri kwa mtsogoleri ku chigawo chakumpoto.

Nawo a Ben Chikhame atenga udindo wa mlembi wa wamkulu wa PP opanda opikisana nawo.

Akuyendetsa zisankho ndi a E.M.J Auditors.

Atolankhani onse awatulutsa chimpinda momwe mukuchitikira zisankho. Dr Joyce Banda, omwe anayamba kuponya voti, akachopa pa malowa, akuti abwerenso kudzatseka msonkhanowu masanawa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tigers’ terror: Massacre at Chichiri Stadium

MBC Online

Anayi ali m’chitokosi ataba mowa wa K2.3 million

Davie Umar

Dr Chakwera apereka ulemu omaliza kwa malemu Dr Chilima ku Nyumba ya Malamulo

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.