Nduna ya maboma ang’ono, Richard Chimwendo Banda, yati boma lipitiriza kuonetsetsa kuti miyoyo ya anthu ammadera akumidzi ikusintha kudzera mu ntchito zachitukuko.
Ndunayi yanena izi ku Makanjira m’boma la Mangochi pamene imayendera zina mwa ntchito zachitukuko zomwe boma likugwira kudzera ku khonsolo ya bomali.
Mwazina, ndunayi pamodzi ndi nduna ya zaumoyo, Khumbize Kandodo Chiponda, yayendera ntchito yomanga bridge ya Lukoloma yandalama zopyola K3 billion, yomwe akuigwira pofuna kuchepetsa mavuto amayendedwe pakati pa anthu oyenda msewu wa Mangochi-Makanjira.
Ndunazi zayenderanso ntchito yomanga chipatala cha Makanjira, yomwe I kuyembekezeka kufika kumapeto mwezi wa January chaka chamawa.
Olemba: Owen Mavula