Mayi wa pfuko lino, Madam Monica Chakwera, atsegulira sukulu yatsopano ya sekondale yoyendera ya mdera la Chiyola m’boma Rumphi imene bungwe la Press Trust lamanga.
Sukuluyi ili ndi zipinda zofunika monga makalasi ophunzirira ngakhalenso chipinda chosungira mabuku.
Themba la Mathemba Chikulamayembe athokoza boma popititsa patsogolo maphunziro m’dziko muno ndipo ati chiyembekezo kuti derali litukuka kwambiri m’magawo osiyanasiyana chifukwa cha sukuluyi.
Iwo atinso atsikana mderali amayenda mtunda wautali kuti akapeze maphunziro ku sukulu za Mwasizi ngakhalenso Katowo.