Mafumu ku Machinjiri m’boma la Blantyre awuza anthu awo kuti akalembetse mayina mu kaundula wachisankho amene akuchititsa a Malawi Electoral Commission (MEC).
M’madera aku Machinjiri, kalemberayu anayamba pa 9 November 2024.
Mafumuwa anati anthuwo akonzekere kudzasankha atsogoleri amene asonyeza chidwi chothandiza kutukula miyoyo yawo.
Mfumu Nathoka ndi Andasani amayankhula poyimira mafumu 21 amene anakhamukira kunyumba kwa ochita malonda, a Alex Chimwala, amene posachedwapa analengeza kuti asiya ndale pofuna kulimbikira bizinesi yawo.
Iwo amakapereka kalata kwa a Chimwala kuti asinthe maganizo awo ndi kudzawayimilira pa chisankho cha aphungu cha chaka cha mawa mdera la South Lunzu.
Malinga ndi mafumuwa, mkuluyo anakonza polisi imene anthu anayiononga m’mbuyomu ndikukonzanso milatho komanso kulipilira fizi ana osowa.