Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani

Lekani kutchetcha chimanga m’minda — Boma lauza LCC

Chinthuzi: Tsamba la mchezo

Unduna wa maboma ang’ono wauza khonsolo ya mzinda wa Lilongwe (LCC) kuti ileke ntchito yotchetcha chimanga mminda ya anthu ena mumzindawu mpaka nkhaniyi itaunikidwa bwino lomwe.

Izi zadza anthu okhala mumzindawu, maka m’madera a Area 43 ndi 11,atadandaula ndi zimene inachita khonsoloyi lachitatu potchetcha chimanga chokulakula mminda yawo, potengera kuti malamulo sakulora anthuwa kulima mmapuloti amderali.

Koma mukalata imene wasayinira mlembi wa mu unduna wa maboma ang’ono, a  James Chiusiwa, boma lati kutsata malamulo kuli apo,ilo lamva kudandaula kwa anthuwa, poganiziranso kuti mwina dziko lino likhoza kukhala ndi chakudya chochepa malinga ndi m’mene nyengo ikuyendera.

Lachitatu, m’modzi mwa akuluakulu a khonsolo ya mzinda wa Lilongwe,a Allan Domingo,anati khonsoloyo yatchetcha kale chimanga mminda yokwana khumi,malinga ndi malamulo awo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Government grants will boost ATM Strategy’

MBC Online

CHAKWERA TO ADDRESS THE NATION WEDNESDAY

MBC Online

DoDMA donates food to orphanage in Mchinji

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.