Bungwe la Action Aid lati likambirana ndi boma kuti lithandize sukulu ya pulayimale ya John C. Thomas kumene kabweredwe ka ophunzira kasintha kutsatira kuthetsa kuphika phala.
M’modzi mwa akuluakulu a bungweli, Dr Chikondi Mpokosa, amayankhula izi atayendera ntchito za sukulu ya mkombaphala ya Mutu CDCC komanso m’mene bungwe lawo lakwezera maphunziro m’mudzi mwa mfumu yaikulu Mtema m’boma la Lilongwe.
Kumeneku, ana ambiri amachokera pa Mutu CDCC ndikupita ku sukulu ya pulayimale ya John C Thomas.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa pasukulu ya John C Thomas, a Mercy Masoatengenji, anati kusiya kuphika phala kwakhudza maphunziro pa sukuluyi kaamba koti ana ambiri akumakhala ndi njala komanso akhala akusonkha okha ndalama ya chakudya cha anawa.
A Masoatengenji ati izi zili chomwechi ngakhale sukulu ya mkombaphalayi yathandiza kwambiri kupititsa patsogolo maphunziro pasukulu yawo.