Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tsopano ndikupeza bwino-Ras Kansengwa

M’modzi mwa akatswiri wotola zithunzi m’dziko muno, Ras Peter Kansengwa, wati tsopano akupeza bwino ku chipatala komwe ali cha Artemis m’dziko la India.

Poyankhula ndi MBC m’mawa wa Lachiwiri, mkuluyu wayamika boma ndi anthu akufuna kwabwino omwe athandizira kuti akapeze thandizo la mankhwala ku dziko la India.

“Mankhwala andipatsa ndithu, sikuti ndadwalika mwakayakaya momwe ena akhala akuganizira ayi ndili bwino ndipo mankhwala ndayambapo ndidzamalizira kumudzi. Madokotala amangoyambapo koma machilitso amamalizitsa ndi mwini wake Mulungu,” watero Kansengwa.

Ras Kansengwa wati amuthandiza kwambiri vuto la miyendo, yomwe yakhala ikumuvuta kwanthawi yayitali.

Ras Kansengwa wati akuyembekezeka kubwelera ku Malawi pa 10 May, 2024.

Iye wakhala aliku chipatala cha Artemis m’dziko la India kwa mwezi umodzi tsopano.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

US govt’s $350M Compact Pack for Malawi rolls into life

MBC Online

‘Social Cash Transfer Programme will reach vulnerable people’

Olive Phiri

Deputy Speaker condemns child marriages

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.