Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Komiti yakunyumba yamalamulo yakhutira ndikuthetsedwa kwa mlandu wa a Chilima

Mkulu ozenga milandu yaboma, a Masauko Chamkakala

Komiti yakunyumba yamalamulo yoona zamalamulo yati yagwirizana ndi zifukwa zomwe mkulu ozenga milandu yaboma, a Masauko Chamkakala, anaathetsera mlandu wa wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima.

Iwo ati mlanduwu  umakhudza chitetezo chadziko ndipo sungabwelere kubwalo lamilandu.

Malinga ndi wapampando wakomitiyi, a Peter Dimba, mlandu omwe ubwelere kubwalo lamilandu pakadali pano omwe mkulu ozenga milandu yaboma m’dziko munoyu adaauthetsa ndiokhudza kampani ya Paramount Holdings.

A Dimba ati umboni omwe a Chamkakala anafotokozera komitiyi kuti athetse mlandu okhudza kampaniyi siogwirika.

Akuluakulu a kampani ya Paramount Holdings amkawaimba mlandu opereka zikalata zabodza kuti apeze mwayi operekera katundu ku nthambi komanso maunduna ena aboma, pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino  amkamuimba mlandu okhudzana ndi katangale.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Karonga has 41 internally displaced households

MBC Online

Anamalira akhamukira ku CI

Blessings Kanache

PRESIDENT CHAKWERA CALLS FOR UNITY AMONG TRIBES

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.