Bwalo la Mkukula Senior Resident Magistrate m’boma la Dowa lalamula nzika yaku Niger, Osman Muhammed, wa zaka makumi atatu kuti alipire chindapusa cha K600,000 chifukwa chopezeka ndi mankhwala ozunguza bongo a diamorphine komanso kufuna kuwatumiza kunja popanda zikalata zovomerezeka.
Malinga ndi mneneri wapa bwalo la ndege la KIA, a Dorrah Machira, Muhammed adamugwira pabwalo la ndegeli atabisa ena mwa mankhwalawa kumalo wobisika kokhalira pa 14 mwezi uno pa ulendo wopita mdziko la Germany.
Malinga ndi a Machira, wapolisi woimira boma pamlandu, Sandra Banda, anauza bwalo bwino lomwe zimene mkuluyu adachita pofuna kutulutsa mankhwala wozunguza bongo m’dziko muno.
Popereka chigamulo, Senior Resident Magistrate Montfort Misunje anagwirizana ndi oimila boma pomwe analamula Muhammed kupeleka chindapusa cha K600,000 pa milandu yonse iwili.
Muhammed wapereka chindapusachi.