Thupi la amene anali mkhalakale pa nkhani zoulutsa mawu, Joshua Kambwiri, alitengera ku mudzi kwawo ku Domasi m’boma la Zomba, kumene akaliyike m’manda mawa Lolemba.
Mwambo wa mapemphero otsanzikana ndi malemu Kambwiri unachitikira pa tchalitchi cha Ngumbe CCAP ku Chileka munzinda wa Blantyre kumene malemuwa amapemphera.
Malemu Kambwiri, amene anagwirapo ntchito ku nyumba youlutsa mawu ya MBC, amwalira ali ndi zaka 62.