Bungwe la Immigration lati pakufunika mgwirizano polimbikitsa aMalawi kuti azitsata malamulo pamene akupita maiko ena.
M’modzi mwa adindo ku bungweli, a Fletcher Nyirenda, anayankhula izi pamasewero osiyanasiyana amene Immigration inakonza ku Lilongwe.
Oona ntchito zothana ndi katangale ku bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB), a Susan Mtuwa Phiri, anali komweko ndipo anaphunzitsa anthu ogwira ntchito ku Immigration zokhudza ziphuphu ndi katangale.
A Phiri anati izi zili chomwechi chifukwa m’chitidwe wa ziphuphu ndi katangale umachitikanso kunthambi zaboma.
Iwo anati ubale wanthambi ziwirizi usangokhala omanga anthu koma wothandizana kupewa m’chitidwe oyipawu kuchitika.
Malipoti akuonetsa kuti nzika zina za dziko lino zakhala zikugwidwa m’dziko la South Africa kaamba kosowa mapepala owayenereza opitira kumeneko.