Ophunzira akale apasukulu ya sekondale ya Bwaila, kudzera mu gulu limene adakhazikitsa la Bwaila Social Welfare, loweruka anakapereka katundu osiyanasiyana kwa anthu ovutika komanso amene ali ndi ulumali m’boma la Lilongwe.
Malinga ndi wapampando wagululi, Martin Makhuyula, katundu yemwe amagawayu, kuphatikizapo njinga, anagulidwa ndi ndalama zimene mamembala awo anasonkha.
Iwo alimbikitsanso Amalawi kuti achilimike pantchito zachifundo chifukwa pali anthu ambiri amene ali ndi zosowa.
Ena mwa anthu amene afikiridwa ndi thandizoli ndi okhala m’madera a Area 36 komanso kwa Nayele.