Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Flames imenya World Cup boma likathandiza moyenera — Haiya

Mtsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM), a Fleetwood Haiya, wati ngati boma lingawapatse thandizo loyenera, Flames ili ndi kuthekera kodzatenga nawo gawo mu mpikisano wa World Cup m’chaka cha 2026.

A Haiya anena izi Lachisanu munzinda wa Lilongwe pamwambo osangalala pamodzi ndi komiti yawo kuti akwanitsa chaka chimodzi akutsogolera bungwe la FAM.

Iwo apemphanso aMalawi kuti apitirize kupereka malangizo oyenera kuti iwo apitirize kuchita bwino ndipo analonjezanso kupitiriza kupititsa patsogolo mfundo zimene zinali mu ndondomeko yawo yokopera anthu.

A Haiya anati m’chaka cha 2025 akuyang’anira zinthu zambiri zothandiza ntchito zokhudza FAM. Mwachitsanzo, iwo anati akhala akudikira thandizo la Flames komanso Scorchers limene limachokera ku nyumba ya malamulo.

Iwo anatinso akufuna kukhazikitsa bwalo loweruza milandu yokhudza mpira wa miyendo, kukhazikitsa migwirizano yovomerezeka ndi mabungwe amene amagwira ntchito ndi FAM komanso kukhazikitsa ofesi za ma bungwe amene ali pansi pa FAM m’zigawo zonse.

Nduna ya zamasewero, a Uchizi Mkandawire, anayamikira utsogoleri wa a Haiya kaamba kakuti umamvera zofuna za anthu.

A Mkandawire analonjezanso kuti boma liyesetsa kuchita mbali yake pothandiza ntchito za FAM komabe iwo anapemphanso bungweli kuti lidzitha kugwiritsa ntchito thandizo limene alipatsa chifukwa sinthawi zonse boma litha kukwanitsa zonse zofuna zawo.

Ndunayi inalangizanso FAM kuti ipititse patsogolo ubale ndi kampani zimene zingathandizane ndi boma powathandiza.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA HOMEBOUND

MBC Online

DRIVERS COMMEND MRA FOR DEDZA ONE-STOP BORDER POST

McDonald Chiwayula

Malawi will face South Africa in COSAFA Beach Soccer opener

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.