FDH Bank yalengeza kuti ithandiza ligi yadziko lonse yamasewero ampira wamanja (Netball) ndi ndalama zokwana K1.2 billion kwa zaka zinayi.
Kotero, chaka chili chonse bankiyi idzipereka K300 million yothandizira mpikisanowu.
Izi walankhula ndi m’modzi mwa akuluakulu a bankiyi, a Noel Mkulichi, pamwambo omwe ukuchitikira munzinda wa Blantyre.
Akuluakulu aku unduna wazamasewero ndi Malawi National Council of Sports ali nawo pamwambowu.
Matimu khumi ndi awiri ndi amene asewere muligiyi ndipo asanu ndi atatu wa iwo ndi amene akhala akuchita bwino mmaligi a m’zigawo. Matimuwa ndi Kukoma Diamonds, Tigresses,Blue Eagles, Civonets ndi Prisons Queens. Ena otsalawo apezeka akachita masewero odzigulira malo.
Matimuwa adzisewera mu magawo awiri pachaka.
Bungwe la NAM lasankhanso komiti yomwe idziyendetsa ligiyi motsogozedwa ndi wapampando, Linda Magombo Munthali.
Mipira ndi zovala zogwiritsidwa ntchito mumpikisanowu adzipereka ndi a bank ya FDH.
Olemba: Praise Majawa