Phungu wa dera la Lilongwe City South East Ulemu Msungama wapempha anthu mdziko muno kuti asiye mchitidwe wa nkhanza kwa amayi.
Iwo amalankhula izi pa sukulu ya Mloza ku Area 23 mu mzinda wa Lilongwe pomwe amapereka nsalu kwa amayi oposera 400 am’dera lawo ngati njira yosangalalira tsiku la anakubala.
A Msungama ati ndi zomvetsa chisoni kuti anthu ena amachitira amayi nkhanza zosiyanasiyana m’malo mowapatsa chisamaliro choyenera.
“Tiyeni pamene lero tikukondwelera tsiku la anakubala tikumbutsane za kuipa kozunza amayi. Uthenga wanga wapadera lero ndioti tisachite nkhanza kwa amayi, tiyeni tiwasamalire,” atero a Msungama.
Kupatula kupereka nsalu, phunguyu waperekanso matumba a mphatso zosiyanasiyana. M’matumbawa munali ufa, shuga, mchere ndi zina. Asanagawe katunduyi, a Msungama anadya nawo limodzi chakudya cha masana amaiwa omwe anabwera ndi mafumu akudelari.