Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wapereka ndalama zokwana K5 million kuti zithandizire pamwambo wa maliro a Raphael Kasambara omwe atisiya masiku apitawa.
A Harry Mkandawire, amene akuyimira Dr Chakwera, ati malemu a Raphael Kasambara anali munthu okonda kumenyera ufulu wa anthu osauka.
Iwo ati boma lisowa ntchito zambiri zomwe malemuwa anathandizirapo maaka pa chitukuko.
A Mkandawrire ayankhula izi pamene mwambo wa maliro uli mkati m’boma la Nkhata Bay.