Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Boma ligula PREP ochuluka chaka chamawa

Boma lati ligula mankhwala ochuluka obaya othandiza kuchepetsa kufala kwa kachilombo ka HIV kumapeto achaka cha 2025 ndicholinga chothadiza pantchito yolimbana ndikufala kwa kachilomboka.

Mkulu oona za kachilombo ka HIV komanso matenda opatsirana pogonana ku unduna wa zaumoyo, Dr Rose Nyirenda, ndiye wayankhula izi pamsonkhano wa atolankhani munzinda wa Lilongwe.

A Nyirenda ati dziko la Malawi linalandira mankhwala obayawa 9,000 amene pakadali pano akuperekedwa muzipatala zisanu ndi chimodzi m’maboma a Lilongwe ndi Blantyre pofuna kuthana ndikufala kwa kachilombo ka HIV mdziko muno.

“Boma ligula mankhwala ochuluka chaka 2025 omwe adzawapereka m’zipatala 41 zam’dziko muno kuti ateteze anthu omwe ali pachiopsezo chotenga kachilombo ka HIV,” atero a Nyirenda.

A Chimwemwe Mablekisi, m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la National Aids Commission (NAC), ati mankhwala obayawa sachilitsa edzi ndipo sateteza kumatenda ena opatsirana pogonana.

Mankhwala obaya othandiza kupewa kutenga kachilombo ka HIV, omwe pachingerezi akuti Pre Exposure Prophylaxis (PrEP), anawakhazikitsa kuno ku Malawi m’mwezi wa September koma ntchito yopereka mankhwalawa inayamba pa 18 March chaka chino.

Dziko la Malawi ndi dziko la chitatu tsopano padziko lonse kuyamba kugwiritsa ntchito makhwala obayawa, pamwamba pamayiko a Zimbabwe ndi Zambia.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHITUKUKO CHIFIKIRE MADERA ONSE — ZIKHALE

MBC Online

BANGWE ALL STARS IN FUNDRAISER

Norbert Jameson

CHAKWERA HOMECOMING MONDAY

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.