Mphunzitsi wa timu ya Flames Patrick Mabedi wasintha malo awosewera awiri mtsiku la lero kusiyana ndi timu yomwe inayamba m’masewero apa bwalo la Bingu ndi timu ya Sao Tome sabata yatha.
Mabedi wakhulupilira ntchito za Patrick Mwaungulu ndi Henri Kumwenda omwe anachita kuchokera panja m’masewero apita.
Masanawa Flames yomwe ili ndi mapointi asanu ndi imodzi ikumana ndi Equatorial Guinea yomwe ilibe pointi ngakhale imodzi atawachotsera mapointi onse kaamba koseweretsa munthu yemwe sanali woyenera kusewera.
Flames ili panambala yachinayi pomwe Equatorial Guinea ndiyachisanu mugululi.