Bungwe la oyimba la Copy right Society of Malawi (COSOMA) lati mawa lipereka ndalama za nkhaninkhani kwa oyimba m’dziko muno kudzera ku thumba la bungwe la Malawi Revenue Authority la Blank Media Levy.
Wapampando wa bodi ya COSOMA, Reverend Chimwemwe Mhango, watsimikiza izi.
“Pali oyimba ambiri amene mawa lino alandira ma million kuposa momwe tinapelekera m’mbuyomu koma nditsindike kuti ndalamazi sitipereka kwa oyimba wina aliyense amene ndi membala wa bungwe la COSOMA koma tipereka kwa oyimba okhawo amene nyimbo zawo anthu akhala akuzigawana pogwiritsa zipangizo za digital monga lamya za m’manja, pa kompyuta komanso pa internet kudzera pa masamba a mchezo,” atero a Mhango.
M’mbuyomu kwakhala kuli maphokoso pa ndondomeko yomwe bungwe la COSOMA limatsata posankha oyimba amene alandire ndalamazi.
Mwambowu uchitikira munzinda wa Lilongwe.